My Daughter Juliet Read Count : 44

Category : Books-Fiction

Sub Category : Historical Fiction

MY MOTHER IS A HERO
##################
" mayo mukundipha ine, mayo ine " anakuwa mayi mchipinda chawo chifukwa choti amuna awo anali akuwamenya kwambiri.. Panthawiyi mkuti John mwana wa mayiwa ali mchipinda mwake koma zomse zomwe zimachitikazi anali akungomvesera, 
" anthu otembeleledwa inu, chomwe ukukanika kundipasa mwana wa nkazi ndi chani? Ine ndikufuna mwana wa Mkazi apo bii ndizikumenya daily wamva" awa ndi bambo Chirwa omwe anali ochokera ku mpoto komwe amasamala kwambiri ana a atsikana kuposa anyamata, 
" koma mukupangilanji zimenezi inuyo? Kodi mmesa ana amapeleka ndi Mulungu? Mukundizumzilanji?" Uku ndikulamkhula kwa mayi ake a John kudandaula ndi nkhaza zomwe amalandika kuchokera kwa amuna awo maka akangomwa mowa,,
Panthawiyi mayi anali akutuluka magazi chifukwa cha zibagera zomwe zimabwera mosalekeza kuchokera kwa amuna awo,,,
Panthawiyi John anali duu ku chipinda chake comwe chinali pafupi ndi cha mayi ake zomwe zimapangisa kuti azimva zomse zomwe zimachitika mchipinda mwa mwayi akewo,,
" ambuye, mchifukwa chani mumalola mayi anga azizumzika choti? Ine ndidakali wamng'ono sindingakwanise kuwathandiza mayi anga, ndipanga bwanji ine?" Uku kunali kudandaula kwa John, amalamkhula izi misomzi ikusika mmasaya mwake, 
Mwana anali ndi mafumso ochuluka osowa nawo mayamkho, 
Bambo ake anali akungokalipilabe mchipinda muja, 
Mayi ake pamsipansi akulira mosisima,
" kwa amzanga omse amakhala bwinobwino koma kwathu kuno mchifukwa chani adad akamwa mowa amangowamenya adad?? Ndizapange bwanji kuti ndizawapulumuse mayi anga?? Mwina ndingolimbikira school, komano kuti ndizamalize school silerotu, mayi anga akhalabe mmavuto mpakana ndimalize school?? Chonde ambuye ndithandizeni ndipanga bwanji ine" uku mkudandaula kwa John, mkati mwake munali mafunso opanda mayamkho,,,
Next
Next 
Next

Comments

  • No Comments
Log Out?

Are you sure you want to log out?